Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 8:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Nthaŵi ya chimalizo yaŵakwanira anthu anga Aisraele, sindidzaŵakhululukiranso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?” Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 8:2
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.


ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.


Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'mizinda imene mwailanda.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu; chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti chitsiriziro chathu chafikadi.


Chifukwa chake unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzautchulanso mwambi mu Israele; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzachitika masomphenya ali onse.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.


Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.


Koma nyumba ya Israele siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israele ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima.


Kutha kwafika, kwafika kutha. Kwakugalamukira, taona kwafika.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.


Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso:


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, dengu la zipatso zamalimwe.


Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.


Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wake mikono makumi awiri, ndi chitando chake mikono khumi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa