Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 7:7 - Buku Lopatulika

7 Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Zina ndi izi zimene Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ndidaona Iye ataima pamwamba pa khoma lomangamanga, m'manja mwake ali ndi chingwe choongolera khoma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 7:7
13 Mawu Ofanana  

Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;


Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.


Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.


Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khwangwala adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu.


Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo; waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.


Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m'dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye.


Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso:


Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.


Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.


Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nao muyeso, bango lagolide, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa