Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 7:16 - Buku Lopatulika

16 Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Nchifukwa chake tsono imva mau amene Chauta akunena. Iweyo ukundiwuza kuti ndisalose zotsutsa Israele, ndisalalike zotsutsa banja la Isaki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti, “ ‘Usanenere zotsutsa Israeli, ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Amosi 7:16
14 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.


Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.


Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.


amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israele onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwaomwao, Tamverani mau a Yehova.


Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova:


Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango yakuthengo la kumwera kwa Yuda;


Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israele kulitsutsa;


Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.


koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.


Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka.


Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.


Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa