Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 7:15 - Buku Lopatulika

15 ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Chauta adachita kukanditenga, kundileketsa ntchito yoŵeta nkhosa, nandiwuza kuti, ‘Pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’

Onani mutuwo Koperani




Amosi 7:15
15 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.


Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.


Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.


Pamenepo Yeremiya ananena kwa akulu onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mzinda uwu mau onse amene mwamva.


Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?


Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.


Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.


Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa