Amosi 7:17 - Buku Lopatulika17 chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Tsono zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Mkazi wako adzasanduka mkazi wadama mumzindamu. Ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa pa nkhondo. Dziko lako adzaligaŵagaŵa kugaŵira anthu ena. Iweyo ukafera ku dziko lachikunja. Ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo kutali ndi dziko lao.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 “Tsono zimene akunena Yehova ndi izi: “ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu, ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa, ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu. Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ” Onani mutuwo |