Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 7:14 - Buku Lopatulika

14 Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Amosi adayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri konse, kapenanso wa m'gulu la aneneri. Inetu ndine woŵeta nkhosa, ndiponso wolima nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 7:14
17 Mawu Ofanana  

Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.


Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha.


Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake.


Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete.


Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete.


Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordani.


Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.


Ndipo ana a aneneri anati kwa Elisa, Taonani tsono, pamalo tikhalapo ife pamaso panu patichepera


Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele.


Atchera therere lokolera kuzitsamba, ndi chakudya chao ndicho mizu ya dinde.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?


koma adzati, Sindili mneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.


koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;


Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa