Amosi 5:3 - Buku Lopatulika3 Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mzinda wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mudzi wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: “Mzinda umene udapita ku nkhondo ndi anthu chikwi udzatsala ndi anthu zana limodzi chabe. Ndipo umene udapita ku nkhondo ndi anthu zana limodzi, udzatsala ndi anthu khumi okha a m'banja la Israele.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.” Onani mutuwo |