Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 3:6 - Buku Lopatulika

6 Kodi adzaomba lipenga m'mzinda osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mzinda osachichita Yehova?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mudzi osachichita Yehova?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kodi lipenga lankhondo nkulira mu mzinda, anthu osachita mantha? Nanga tsoka likagwera mzinda, kodi si Chauta amene amachita zimenezo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda, anthu sanjenjemera? Pamene tsoka lafika mu mzinda, kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:6
17 Mawu Ofanana  

Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.


Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?


Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi.


Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Nenani mu Yuda, lalikirani mu Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'mizinda ya malinga.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


nakaona iye lupanga lilikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kuchenjeza anthu;


Ombani mphalasa mu Gibea, ndi lipenga mu Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.


Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu?


tsiku la lipenga ndi lakufuulira mizinda yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungodya.


Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.


ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.


Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa