Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 3:1 - Buku Lopatulika

1 Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Imvani mau amene Chauta adalankhula, mau okudzudzulani inu Aisraele, ndiye kuti banja lonse limene Iye adalitulutsa ku dziko la Ejipito. Adanena kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:1
18 Mawu Ofanana  

Inu mbeu ya Israele mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake.


nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala mu Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.


Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani chibadwire;


Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza.


Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.


Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.


Ndipo otsala onse amene akutsala pa banja loipa ili adzasankha imfa koposa moyo, ndiwo amene atsala m'malo monse m'mene ndinawaingiramo, ati Yehova wa makamu.


Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.


Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.


Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.


Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa.


Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo?


Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa