Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 8:8 - Buku Lopatulika

8 Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena, Taonani, akudza masiku, anena Ambuye, Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena, Taonani, akudza masiku, anena Ambuye, Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma Mulungu adadzudzula anthu ake ndi mau aŵa akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzachita chipangano chatsopano ndi fuko la Israele, ndiponso ndi fuko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati, “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachita pangano latsopano ndi Aisraeli ndiponso nyumba ya Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 8:8
25 Mawu Ofanana  

Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.


Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito;


Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.


ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere.


Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.


pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wa chipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.


Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona.


Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.


Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano.


Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa.


amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.


Koma sindichita chipangano ichi ndi lumbiro ili ndi inu nokha;


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa.


Pakunena Iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma chimene chilinkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.


Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.


Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa