Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 8:9 - Buku Lopatulika

9 losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalebe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalire iwo, anena Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalabe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalira iwo, anena Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Sichidzakhala chonga chipangano chimene ndidaachita ndi makolo ao tsiku limene ndidaachita kuŵagwira pa dzanja kuti ndiŵatulutse m'dziko la Ejipito. Chifukwa iwo sadasunge chipangano changa chija, nanenso sindidaŵasamale”, akutero Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo, pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija ndipo Ine sindinawasamalire, akutero Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 8:9
44 Mawu Ofanana  

Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mzinda.


Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro; kapena kugwiriziza ochita zoipa.


Potero anatulutsa anthu ake ndi kusekerera, osankhika ake ndi kufuula mokondwera.


Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa, ndi dzanja la Mose ndi Aroni.


koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda.


wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.


Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitike zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.


Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe, pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.


Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana aamuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.


M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.


si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.


Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzachita ndi iwe monga umo unachitira; popeza wapepula lumbiro ndi kuthyola pangano.


Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.


Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.


Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.


Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?


Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenye kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye mu Damasiko.


pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.


Awa ndi mau a chipangano chimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m'dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao mu Horebu.


kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino;


Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa