Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Malamulo a Mose amati ana a Levi, amene ali ansembe, azilandira chachikhumi kwa Aisraele. Ndiye kuti iwo amalandira kwa abale ao, ngakhale abalewo nawonso ndi ana a Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:5
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;


Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo mu Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;


Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.


Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake.


Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali mu Ejipito.


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.


Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.


Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.


pakuti pajapo anali m'chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa