Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 6:8 - Buku Lopatulika

8 koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma ngati ibereka minga ndi nthula, ndi yachabe ndipo ili pafupi kutembereredwa. Mathero ake nkutenthedwa m'moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma nthaka yobereka minga ndi nthula ndi yopanda phindu ndipo ili pafupi kutembereredwa. Matsiriziro ake idzatenthedwa mʼmoto.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 6:8
26 Mawu Ofanana  

Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira padzanja lako mwazi wa mphwako:


namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pantchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova;


koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.


imere minga m'malo mwa tirigu, ndi dawi m'malo mwa barele. Mau a Yobu atha.


Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? Ndiziponde ndizitenthe pamodzi.


Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu.


Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.


nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uliwonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uliwonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto.


Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva.


Ndipo Petro anakumbukira, nanena naye, Rabi, onani, wafota mkuyuwo munautemberera.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


Ndipo Yehova anawazula m'nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi mu ukali waukulu, nawaponya m'dziko lina, monga lero lino.


koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.


Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa