Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 4:7 - Buku Lopatulika

7 alangizanso tsiku lina, ndi kunena mu Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 alangizanso tsiku lina, ndi kunena m'Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nchifukwa chake Mulungu adaikanso tsiku lina, lotchedwa kuti “Lero”. Patapita nthaŵi yaitali Mulungu adalankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide ponena mau aja tatchula kaleŵa, akuti, “Lero, mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 4:7
12 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.


Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!


Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena,


Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.


Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalimo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja langa lamanja,


Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.


iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwe m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.


Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,


umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa