Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 4:3 - Buku Lopatulika

3 Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ife okhulupirirafe tikuloŵamo mu mpumulowo. Paja Mulungu adaanena kuti, “Ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ” Adaanena zimenezi, ngakhale anali atatsiriza ntchito zake zonse za kulenga dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 4:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.


Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.


chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.


amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.


Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


Monga ndinalumbira mu ukali wanga: Ngati adzalowa mpumulo wanga!


pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;


chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.


amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa