Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 4:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindula nao mau omvekawo, popeza sanasanganizika ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 4:2
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.


Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.


Pakuti inde mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa.


Nanga bwanji ngati ena sanakhulupirire? Kodi kusakhulupirira kwao kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu?


Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.


Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?


Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.


koma mudziwa kuti m'kufooka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba:


Koma m'chinthu ichi simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,


kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.


Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowemo chifukwa cha kusamvera,


Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa