Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 4:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Paja munthu woloŵa mu mpumulo umene Mulungu adalonjeza, nayenso amapumula, kuleka ntchito zake, monga momwe Mulungu adaapumulira, kuleka ntchito zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 4:10
9 Mawu Ofanana  

Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.


Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


koma Iye, m'mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire;


Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.


Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.


Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa