Ahebri 3:9 - Buku Lopatulika9 chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mulungu akuti, Pamene paja, makolo anu adaandiputa pakundiyesa, ndipo adaona zimene ndidaŵachita pa zaka makumi anai. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa, ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.