Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 13:23 - Buku Lopatulika

23 Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Ndikufuna kuti mudziŵe kuti Timoteo, mbale wathu, amtulutsa m'ndende. Akafika msanga, ndidzabwera naye kwanuko podzakuwonani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ine ndikufuna kuti inu mudziwe kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa. Ngati iye angafike msanga ndibwera naye kudzakuonani.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 13:23
10 Mawu Ofanana  

Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndilikutumikira oyera mtima.


Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzapyola kwanu kupita ku Spaniya.


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,


ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu mu Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;


Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.


Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;


Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu,


Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa