Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 10:6 - Buku Lopatulika

6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwere nazo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwera nazo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Nsembe zoocha kwathunthu ndi nsembe zoperekera machimo, simudakondwere nazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Simunakondwere nazo nsembe zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 10:6
9 Mawu Ofanana  

Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapemphe.


Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa