Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 4:9 - Buku Lopatulika

9 Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono mau akuti “adakwera” tanthauzo lake nchiyani? Ndiye kuti poyamba adaatsikira pansi penipeni pa dziko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kodi mawu akuti, “Iye anakwera” akutanthauza chiyani, ngati Iyeyo sanatsikire kunsi kwa dziko lapansi?

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 4:9
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mzinda ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu.


Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi.


Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge, adzalowa m'munsi mwake mwa dziko.


Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu, munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.


Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.


Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.


Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.


kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala mu Mwambayo.


Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.


Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.


Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.


Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.


Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse.


Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?


Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako.


Munamchepsa pang'ono ndi angelo, mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuika iye woyang'anira ntchito za manja anu;


Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa