Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 4:8 - Buku Lopatulika

8 Chifukwa chake anena, M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chifukwa chake anena, M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Paja mau a Mulungu akuti, “Pamene adakwera Kumwamba, adatenga chigulu cha am'ndende, ndipo adagaŵira anthu mphatso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Nʼchifukwa chake akunena kuti, “Iye atakwera kumwamba, anatenga chigulu cha a mʼndende ndipo anapereka mphatso kwa anthu.”

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 4:8
7 Mawu Ofanana  

Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akulu ake onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.


Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.


Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.


Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;


atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.


Galamuka, Debora, galamuka, galamuka, galamuka, unene nyimbo; uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe.


Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa