Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 3:14 - Buku Lopatulika

14 Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate,

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 3:14
16 Mawu Ofanana  

Ndiponso ndidasiya mu Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.


Ndipo kunali kuti atatsiriza Solomoni kupemphera kwa Yehova pemphero ndi pembedzero lino lonse, ananyamuka ku guwa la nsembe la Yehova pomwe analikugwada pa mabondo ake, ndi manja ake otambasulira kumwamba.


Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m'litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba;


Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;


Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.


Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,


Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.


Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,


Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.


Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alitcha dzina,


kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa