Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Timoteyo 2:5 - Buku Lopatulika

5 Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesana monga adapangana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Munthu wothamanga pa mpikisano wa liŵiro, sangalandire mphotho ngati sathamanga motsata malamulo a mpikisanowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Chimodzimodzinso, munthu amene ali pa mpikisano waliwiro, salandira mphotho ya wopambana pokhapokha atatsiriza monga mwa malamulo a mpikisanowo.

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 2:5
14 Mawu Ofanana  

Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.


Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndeu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima;


kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.


Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo tchimo;


Munamchepsa pang'ono ndi angelo, mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuika iye woyang'anira ntchito za manja anu;


Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako.


akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,


Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa