2 Timoteyo 1:5 - Buku Lopatulika5 pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa agogo ako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe. Onani mutuwo |