2 Samueli 3:29 - Buku Lopatulika29 chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 chilango chigwere pa mutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Mlandu umenewu ugwere Yowabu ndi onse a pa banja la bambo wake. Ndipo Mulungu amlange Yowabuyu kuti pabanja pake pasadzakhale popanda munthu wa nthenda ya chidzonono, kapena wakhate, kapena wolumala, kapena wophedwa ku nkhondo kapenanso wosoŵa chakudya.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Mlandu umenewu ukhala pa Yowabu ndi banja lonse la abambo ake! Mʼbanja la Yowabu musadzasowe munthu wodwala matenda a chizonono kapena khate, kapena wolumala woyendera ndodo kapena wophedwa ndi lupanga, kapena wosowa chakudya.” Onani mutuwo |