Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 3:21 - Buku Lopatulika

21 Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono Abinere adauza Davide kuti, “Loleni ndikasonkhanitse Aisraele onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuyanga mfumu, kuti adzachite nanu chipangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Choncho Davide adamlola Abinere kuti apite. Ndipo iye adapita mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndipo Abineri anawuza Davide kuti, “Loleni kuti ndipite msanga kukasonkhanitsa Aisraeli onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuye wanga mfumu, kuti adzachite nanu pangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Kotero Davide analola Abineri kuti apite, ndipo anapita mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:21
8 Mawu Ofanana  

namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.


kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.


Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.


Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero.


Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.


Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzachita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israele.


likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse.


Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa