Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 3:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Nthaŵi yomweyo ankhondo a Davide adafika ndi Yowabu kuchokera kumene adaakamenya nkhondo, atatenga zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ndi Davide ku Hebroni, popeza kuti anali atamlola kuti apite, ndipo iye anali atapitadi mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Nthawi yomweyo ankhondo a Davide ndi Yowabu anafika kuchokera kumene anakathira nkhondo ndipo anabweretsa katundu wambiri wolanda ku nkhondo. Koma Abineri sanalinso ndi Davide ku Hebroni, chifukwa Davide anamulola kuti apite, ndipo anapita mu mtendere.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:22
3 Mawu Ofanana  

Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere.


Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;


Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa