2 Samueli 20:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Yowabuyo adadza pafupi ndi mkaziyo, ndipo mkazi uja adamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu aYowabu?” Yowabu adayankha kuti, “Ndine amene.” Mkaziyo adamuuza kuti, “Pepani bambo, mumvere mau anga.” Apo Yowabu adayankha kuti, “Inde, ndilikumva!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.” Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.” Onani mutuwo |