Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 2:27 - Buku Lopatulika

27 Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Yowabu adayankha kuti, “Ndithudi, ndikulumbira, pali Mulungu wamoyo, ukadapanda kulankhula, ankhondo angaŵa sakadaleka kuŵathamangitsa abale aowo mpaka maŵa m'maŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Yowabu anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, ukanapanda kuyankhula, ankhondo anga akanapitiriza kuthamangitsa abale awo mpaka mmawa.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:27
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire.


Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?


Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso.


Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine, ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga,


Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.


Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.


Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo.


Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.


Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalire izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake.


Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa