2 Samueli 2:26 - Buku Lopatulika26 Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Tsono Abinere adafuulira Yowabu namufunsa kuti, “Kodi tipitirirebe kumenyana mpakampaka? Monga sukudziŵa kuti mathero ake adzakhala oŵaŵa? Kodi udzaŵaletsa liti anthu ako kutithamangitsa ife abale ao?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Abineri anayitana Yowabu, “Kodi tipitirize kumenyana mpaka kalekale? Kodi sukuzindikira kuti mathero ake kudzakhala kuwawidwa mitima? Kodi udzawaletsa liti ankhondo ako kuthamangitsa abale awo?” Onani mutuwo |