2 Samueli 18:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mwadzidzidzi Abisalomu adakumana ndi ankhondo a Davide. Abisalomuyo anali atakwera pa bulu wake, ndipo buluyo adaloŵa kunsi kwa nthambi zochindikira za mtengo wa thundu. Pamenepo Abisalomu adatsalira ali lendee, mutu wake utapanika pa nthambiyo, pamene bulu ankakwerayo adapitirira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Tsono zinachitika kuti Abisalomu anakumana ndi asilikali a Davide. Iye anali atakwera bulu ndipo pamene buluyo amadutsa pansi pa nthambi zambiri za mtengo wa thundu, mutu wa Abisalomu unakodwa mu mtengomo. Iye anasiyidwa atatsakamira mʼmalele, pamene bulu amene anakwerapoyo amapitirira. Onani mutuwo |