2 Samueli 15:10 - Buku Lopatulika10 Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Koma Abisalomu adatuma amithenga m'seri kwa mafuko onse a Aisraele kukanena kuti, “Malinga mukangomva kulira kwa lipenga, munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu ya ku Hebroni.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ndipo Abisalomu anatuma amithenga ake mwamseri kwa mafuko onse a Israeli kukanena kuti, “Mukangomva kulira kwa malipenga pamenepo munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu mu Hebroni.’ ” Onani mutuwo |