Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Abisalomu popita, adatenga anthu okwanira 200 a ku Yerusalemu. Iwoŵa anali alendo oitanidwa chabe, mwakuti ankangopita osadziŵa chilichonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Anthu 200 ochokera mu Yerusalemu anapita naye Abisalomu. Iwo anayitanidwa monga alendo ndipo anapita osadziwa chilichonse pa nkhaniyi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:11
8 Mawu Ofanana  

Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi.


Wachibwana akhulupirira mau onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.


Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.


mutafika m'mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa