2 Samueli 13:32 - Buku Lopatulika32 Ndipo Yonadabu mwana wa Simea mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana aamuna a mfumu, pakuti Aminoni yekha wafa, pakuti ichi chinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anachepetsa mlongo wake Tamara. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 Ndipo Yonadabu mwana wa Simea mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Aminoni yekha wafa, pakuti ichi chinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anachepetsa mlongo wake Tamara. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Koma Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide, adati, “Mbuyanga, musaganize kuti ana onse a inu mfumu aphedwa, Aminoni yekha ndiye waphedwa. Zimenezi zachitika poti nzimene Abisalomu adaatsimikiziratu kale, kuyambira pa tsiku limene Aminoni adakakamiza Tamara, mlongo wa Abisalomu, kuchita naye zoipa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara. Onani mutuwo |