Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:24 - Buku Lopatulika

24 Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Adapita kwa mfumu nati, “Amfumu, ine mtumiki wanu ndikukachita ntchito yometa nkhosa ndi anthu anga. Ndimati ngati nkotheka mudzakhale nafe inuyo amfumu pamodzi ndi atumiki anu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:24
8 Mawu Ofanana  

Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu.


Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.


Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititse manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa