Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Patapita zaka ziŵiri zathunthu, Abisalomu anali ndi anthu ake ku ntchito yometa nkhosa ku Baala-Hazori pafupi ndi Efuremu. Tsono adaitana ana aamuna onse a mfumu kuti akakhaleko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:23
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake.


Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.


Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu kazembe wa nkhondo; koma Solomoni mnyamata wanu sanamuitane.


Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.


Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu;


Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.


Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.


Hazori, Rama, Gitaimu,


Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele.


Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.


Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake.


Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititse manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa