Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 12:19 - Buku Lopatulika

19 Koma pamene Davide anaona anyamata ake likunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ake, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma pamene Davide anaona anyamata ake likunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ake, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Koma pamene Davide adaona kuti atumiki ake akunong'onezana, adadziŵa kuti mwana uja wafa. Choncho adafunsa atumiki ake aja kuti, “Kodi mwana uja watisiya?” Atumikiwo adati, “Inde, watisiyadi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?” Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 12:19
4 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga?


Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.


Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, chifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Aminoni.


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa