2 Samueli 12:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mwanayo adamwalira. Atumiki a Davide adaopa kukamuuza kuti mwanayo wafa. Adati, “Pamene mwanayo anali moyo, tinkalankhula naye Davide, koma sankatimvera. Tsono tingathe kukamuuza bwanji lero kuti mwana wafa? Mwina nkudzipweteka.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.” Onani mutuwo |