Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 11:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 11:4
13 Mawu Ofanana  

Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.


Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde.


Pakuona mbala, uvomerezana nayo, nuchita nao achigololo.


Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.


Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.


Usamasendera kwa mkazi kumvula pokhala ali padera chifukwa cha kudetsedwa kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa