Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 1:6 - Buku Lopatulika

6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda paphiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mnyamata wodzanena uja adati, “Zidangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa. Kumeneko ndidaona Saulo atangoti zyoli ku mkondo wake. Nthaŵi imeneyo nkuti magaleta ankhondo, ndiponso adani okwera pa akavalo atamuyandikira Sauloyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:6
9 Mawu Ofanana  

Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.


Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa?


Ndipo iye pakucheukira m'mbuyo mwake anandiona, nandiitana. Ndipo ndinayankha, Ndine.


Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina.


Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki.


Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.


Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa