Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 3:4 - Buku Lopatulika

4 Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chipinda chapoloŵera, m'litali mwake chinali cha mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali wa mamita 54. Nyumbayo m'kati mwake adaikuta ndi golide weniweni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Chipinda cha polowera mulitali mwake chinali mamita asanu ndi anayi ofanana ndi mulifupi mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali mamita 54. Iye anakuta nyumbayo mʼkati mwake ndi golide woyengeka bwino.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 3:4
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.


Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira kuchipinda cholowera cha nyumba ya Yehova tsiku lachisanu ndi chitatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi.


Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko.


Ndipo Yesu analikuyendayenda mu Kachisi m'khonde la Solomoni.


Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.


Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa