Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 3:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo maziko adawaika Solomoni akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wake, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo maziko adawaika Solomoni akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wake, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nyumba ya Chautayo, miyeso yake imene Solomoni adaapereka inali iyi: Potsata miyeso yakale, m'litali mwake inali ya mamita 27, ndipo m'mimba mwake inali ya mamita asanu ndi anai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Maziko amene Solomoni anayika pomanga Nyumba ya Mulungu ndi awa: Mulitali munali mamita 27, mulifupi munali mamita asanu ndi anayi (potsata miyeso yakale).

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 3:3
5 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.


Nayamba kumanga tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri, chaka chachinai cha ufumu wake.


Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m'litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa