Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 13:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Abiya adanyamuka kupita ku nkhondo atatenga gulu lake la ankhondo olimba mtima okwanira 400,000 osankhidwa. Yerobowamu adandanditsa ankhondo ake oti amenyane ndi Abiya, anthu okwanira 800,000, amphamvu ndi osankhidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Abiya anapita ku nkhondo ndi asilikali odziwa bwino nkhondo 400,000, ndipo Yeroboamu anandandalitsa ankhondo, asilikali 800,000 odziwa bwino nkhondo, osankhidwa ndi amphamvu, woti amenyane naye.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 13:3
9 Mawu Ofanana  

Ndipo machitidwe ake ena a Abiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.


Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.


Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu.


Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.


Ndipo Abiya anaimirira paphiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efuremu, nati, Mundimvere Yerobowamu ndi Aisraele onse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa