Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 13:2 - Buku Lopatulika

2 Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zitatu. Mai wake anali Maaka, mwana wa Uriyele wa ku Gibea. Tsono panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka zitatu. Dzina la amayi ake linali Maaka mwana wa Urieli wa ku Gibeya. Koma panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 13:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.


Ndipo masiku akukhala Yerobowamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye ndi makolo ake, nalowa ufumu m'malo mwake Nadabu mwana wake.


Anakhala mfumu zaka zitatu mu Yerusalemu, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu.


Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti.


Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.


Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.


ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.


Napitirira iwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibea, ndiwo wa Benjamini.


Ndipo taonani, munthu nkhalamba anachokera ku ntchito yake kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efuremu, nagonera ku Gibea; koma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.


Ndi Saulo yemwe anamuka kunyumba yake ku Gibea; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa