Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 9:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham'katimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham'katimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ukakafika, ukafunefune Yehu, mwana wa Yehosafati, mdzukulu wa Nimisi. Utampeza ukamuuze kuti achokepo pakati pa anzake, ndipo ukaloŵe naye m'chipinda cham'kati.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 9:2
7 Mawu Ofanana  

Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mzinda, m'chipinda cha m'katimo.


Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m'chipinda cha pakati kubisala.


Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake.


Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu;


Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka.


Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa