2 Mafumu 8:9 - Buku Lopatulika9 Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za mu Damasiko, zosenza ngamira makumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamira makumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Motero Hazaele adapita kukakumana ndi mneneri Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso ndi zinthu zokoma zosiyanasiyana za ku Damasiko. Atafika, adakaima pamaso pa Elisa, munthu wa Mulungu uja, nati, “Munthu wanu Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, wandituma kuti ndikufunseni kuti, kodi ati adzachira?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ” Onani mutuwo |
Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,