2 Mafumu 8:8 - Buku Lopatulika8 Niti mfumu kwa Hazaele, Tenga chaufulu m'dzanja lako, nukakumane naye munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzachira kodi nthenda iyi? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Niti mfumu kwa Hazaele, Tenga chaufulu m'dzanja lako, nukakumane naye munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzachira kodi nthenda iyi? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 idauza Hazaele nduna yake yaikulu kuti, “Tenga mphatso, upite kukakumana naye munthu wa Mulunguyo. Tsono upemphe nzeru kwa Chauta kudzera mwa iyeyo kuti, ‘Kodi mfumu idzachira matenda ameneŵa?’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 inawuza Hazaeli kuti, “Tenga mphatso ndipo pita ukakumane ndi munthu wa Mulungu. Ukandifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ” Onani mutuwo |
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.