Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 7:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kenaka akhate aja adayamba kuuzana kuti, “Ife sitikuchita bwinotu pamenepa. Lero ndilo tsiku limene tili ndi uthenga wabwino kwambiri! Tikakhala chete ndi kumadikira mpaka m'maŵa, tidzalangidwa. Nchifukwa chake tsono tiyeni tikauze nduna za mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 7:9
14 Mawu Ofanana  

Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.


Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.


Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?


Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.


Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.


Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.


Poyamba Ine ndidzati kwa Ziyoni, Taona, taona iwo; ndipo ndidzapereka kwa Yerusalemu wina, amene adza ndi mau abwino.


Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.


Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.


Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.


Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse;


munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa