2 Mafumu 7:10 - Buku Lopatulika10 Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Motero adapita ku Samariya nakaitana alonda a pa chipata cha mzinda naŵauza kuti, “Ife tidaapita ku zithando za Asiriya, ndipo tidangoona kuti kulibe munthu ndi mmodzi yemwe. Ngakhale kumva mau sitidamve, koma tidangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire, ndiponso mahema monga momwe adaaliri.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.” Onani mutuwo |